M’modzi mwa omenyera ufulu wa amayi mdziko lino a Emma Kaliya walangiza Tuno, kuti sakuyenera kusiya kuyimba kapena kuchoka pa masamba a mchezo kamba ka zomwe ena akumunyoza.

A Kaliya ayankhula izi potsatira zomwe oyimbayu walengeza pa tsamba lake la mchezo, kuti wasiya kuyimba komanso achoka pa masamba a mchezo kamba ka kuchuluka kwa anthu omwe akumunyoza chifukwa cha mawonekedwe komanso thupi lake.

A Kaliya ati: “Ndikanakhala ine sindinakasiya kuyimba. Iyeyo samayenera kusiya. Pamenepo mpamene umawawonetsa anthu kuti ndiwe olimba mtima, kuti sungalephere kukwanilitsa zomwe umafuna kamba koti ena akukunyoza. Ukachoka ndekuti tsogolo lako lonse loyimba latha.
“Komanso mukayiwona bwino nkhaniyi zikhoza kutheka kuti nkhanzazi zuchokera mkati mwawo, okha okha oyimbawa. Patha kukhala kuti pali oyimba ena omwe amatuma anthu kuti azinyoza oyimba anzawo.”
Tuno wati nkhanzazi zachitika kwa sabata yonseyi, koma zafika posauzana dzulo pomwe anayimba kuphwando lamayimbidwe lomwe linali ku Silver Stadium
[simple_comments]
Comments
- Jane: A Malawi panyopawo ndithu munthu mpaka adziphe? 😢

